
1 | Timagwira ntchito chifukwa Mulungu akugwira ntchito
Mulungu wakulenga iwe kukhala watsopano. Tsono timamvera Mulungu chifukwa timamukonda Mulunguyo, ndipo timamumvera, Mulungu amagwira ntchito mwaife.
Mulungu wakulenga iwe kukhala watsopano. Tsono timamvera Mulungu chifukwa timamukonda Mulunguyo, ndipo timamumvera, Mulungu amagwira ntchito mwaife.
Ubatizo ndi njira yoyambirira ya kumvera monga mKhristu watsopano. Uma onetsera kwa aliyense yemwe alikunja zomwe Mulungu wachita kuti mwa munthu.
Kudzera mupemphero, timamva umwana wathu mubanja la Mulungu. Yesu anatiphuzitsa momwe tikuyenerera kupemphera munjira yomwe ikuyenerera ku pereka ulemerero kwa Mulungu.
Kudzera mukuwerenga Baibulo, timamva Mulungu akuyakhula nafe. Khalani ndi dogosolo lakawerenge ka Baibulo komanso yambani kuwerenga.
Timasokhana pamodzi kuti tipembeze ndi cholinga choti tithandizone wina ndi nzake kukula musinkhu mwa Khristu. Tikuyenera kukhala ndi chikhalidwe chopembera ndi mpingo umodzi nthawi zonse.
Timapereka chifukwa Mulungu anatipatsa ife Mwana wake. Tikuyenera kukhala ndi dogosolo la kupereka kwathu komanso tikuyenera kupeka wokondwera.
Mulungu akuyitana mKhristu wina aliyense kukhala mboni ya Yesu. Kuchitira umboni wokhudzana ndi Yesu ndi kosavunga monga kuyakhula nkhani yako ndi nkhani ya Mulungu.
Dziko lidzadziwa kuti ndife ana aMulungu kudzera mu chikondi chathu. Baibulo likutilamulira ife kuti tikonde Mulungu, anasi utuu, wina ndi m’dzake, adani athu, komanso iwu omwe ndi osowa.
Pamene Mulungu anakupangani kukhala atsopano, anayamba kupanga banja lanu kukhanso latsopano. Pangani Mulungu ku khala Mulungu wa banja lanu kudzera mukupembeza kwa banja.
Ana a Mulungu si a ngwiro. Amatha nthawi zina kuchimwa koma ana a Mulungu amavomereza matchimo awo ndipo amafunafuna kupha machimo awo kuchokera ku mizu po khonzanso malingaliro awo ndikuvala munthu watsopano.
Imfa ya Yesu siikutitsimikizira kupindula. Akhirisitu amavutika. Koma kuvutika kumeneku ndi kuyesedwa kwa chikhulupiliro chawo. Iwo amene amakhulupiliradi sangataye chiphulumutso chawo konse, komano chikhulupiliro choonadi chimazindikirika pamene akhalabe okhulipirika mpaka kumapeto.
Dr. Hutchens ndi m’busa yemwe anayambitsa Mpingo wa Gospel Life Baptist komanso ndi Mtsogoleri wa Euro-African Baptist Mission, bungweri liri ku zomba Malawi. Dr Hutchens watumikirapo mipingo iwiri mu mzinda wa United States ndipo ali ndi Ph.D. mu maphunziro otchedwa Biblical Theology kuchokera ku The Southern Baptist Theological Seminary. Iye ndi mkazi wake Stacy ali ndi ana asanu.
“Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.”
2 Akorinto 5:17