
1 | Minda Inayi
Cholinga chathu ndikupanga ophunzira ndipo timapanga ophunzira polalikira uthenga wabwino ndi kudzala mipingo. Kuti tidzale mpingo timayenera kukonza munda, kudzala mmunda, kusamalira munda kenaka kukolola mmunda.
Cholinga chathu ndikupanga ophunzira ndipo timapanga ophunzira polalikira uthenga wabwino ndi kudzala mipingo. Kuti tidzale mpingo timayenera kukonza munda, kudzala mmunda, kusamalira munda kenaka kukolola mmunda.
Timakhonza munda watsopano wodzalapo mpingo kudzera mupemphero. Timamupempha Mulungu kuti akonzekeretse nthaka yoti ilandire mbewu ya uthenga wa bwino. Koma tikuyeneranso kuzikonzekeretsa tokha popanga kafukufuku wa munda, kufunafuna munthu wamtendere, ndi kupanga ndondomeko zokaphunzitsa uthenga wabwino.
Kudzala kachisi wa tsopano kuchokera mubaibulo, tikuyenera kudzala munda ndi mbewu ya uthenga wa wabwino. Izi zimafunika kuti tifalitse uthenga wa bwino momveka bwino komanso kwa anthu ambiri. Pamene tifalitsa uthenga wa mulungu, Yesu akutiuza kuti tiyembekeze mayankho anayi (Marko 4:11-20).
Pamene talalikira uthenga wabwino ndikuphunzitsa okhulupirira atsopano, ndi nthawi yoti tiwakhonzekeretse okhulupirira atsopano kuti akhale mpingo. Mpingo umakhala ndi anthu omwe ndi ziwalo ndipo amasonkhana pamodzi kuti amve ulaliki wa baibulo. Mpingowo umachita ubatizo ndi mgonero wa ambuye ndipo umatsogozedwa ndi abusa ndi atumiki.
Dr. Hutchens ndi m’busa yemwe anayambitsa Mpingo wa Gospel Life Baptist komanso ndi tsogoleri wa Euro-African Baptist Mission, bungweri liri ku zomba Malawi. Dr. Hutchens watumikirapo mipingo iwiri ku United States ndipo ali ndi Ph.D. mu maphunziro otchedwa Biblical Theology kuchokera ku The Southern Baptist Theological Seminary. Iye ndi mkazi wake Stacy ali ndi ana asanu.
“Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine. Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera, ndi kuwamphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”
Mateyu 28:18–20