
Kutsindikizidwa ndi Mzimu Woyera
Mulungu watitsindikiza ndi Mzimu Woyera kutitsimizira kuti chipulumutso chathu ndi chamuyaya. Komanso kuti madalitso onse achipulumutso athu tizalandi kutsogolo.
Mbusa Dzimbiri amatsogolera kapembezedwe ku Mpingo wa Gospel Life Baptist komanso amatumikira alimodzi ndi Euro-Africa Baptist Mission yomwe yiri ku Zomba Malawi. M’busa Dzimbiri watumikira mipingo ya ku Malawi komanso ya ku Zambia, ndipo ali ndi M.A. mu maphunziro a zautumiki kuchokera ku Central Africa Baptist University ndi Piedmont International University.
Mulungu watitsindikiza ndi Mzimu Woyera kutitsimizira kuti chipulumutso chathu ndi chamuyaya. Komanso kuti madalitso onse achipulumutso athu tizalandi kutsogolo.
Oyera mtima apirira muchikhulupiriro chawo chifukwa imfa ya Yesu yachotsa chostutsa china chilichonse komanso mlandu uliwonse otsutsana ndi sosakhidwa a Mulungu. Chiukitso cha Yesu ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro chathu komanso mpemphero ake opemperera oyera mtima amatsimikizira kuti chikhulupiriro cho sichifowoka.
Chifukwa cha mphamvu za Mulungu ndi chifuniro chake, anthu woyera mtima apirira mu chikulupirira chawo mpaka kumapeto kwa moyo.
2 Timoteyo 1:9. Kupirira kwa anthu wokhulupirira kwa khazikika mu chikondi chosatha cha Mulungu, yemwe anatipatiratu chisomo chake mwa Yesu Khristu kutiwombola ife ku machimo athu.
Aefeso 1:4–7; Aroma 8:29–30. Chipulumutso ya oyera mtima china yamba ndi Mulungu, ndipo chidzamulizidwa ndi Mulungu. Chifukwa choti Mulungu amatsiriza ndogosolo lomwe wa liyamba adzatsirizanso dogosolo la chipulumutso cha oyera mtima.
“Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.”
2 Petro 3:18