Mulungu ndi odziwa zonse ndi wamphamvu/God is all knowing and all powerful

Gawani

Genesis 18:1-15 Kodi pali chimene ndi chokanika kwa mulungu? Akhristu nthawi zina timayetsedwa kuganiza kuti tili ndi kuthekera komuuza mulungu zomwe iye samadziwa. Koma kodi izi ndi zotheka? M’buku la Genesis 18 likutionetsera kuti mulungu ndi odziwa zonse ndi wamphamvu. Zonse zimene Abrahamu ndi Sara akudutsa ndi njira imene mulungu wayika kuti awiriwa amudziwe mulungu. Mulungu akudziwa pamene Sara anaseka mulungu atanena kuti azakhala ndi mwana ngakhale Sara sanali pafupi ndi ambuye omwe anabwera kwa Abrahamu ndi angelo awiri. Ndi mavuto anji, ndi mtenda yanji kapena ndi chiyani chikusowetsa mtendere moyo wanu? Dziwani kuti zonsezi timadutsa ndi cholinga choti mulungu adzivumbulutse yekha kwa ife momwe anachitira ndi Abrahamu. Kodi inu mudalira mulungu?

Genesis 18:1-15 Is anything impossible for God? Christians sometimes are tempted to think that they can tell God what they think he doesn’t know about them. Is that even possible? Genesis 18 tells us that God is all knowing and all powerful. All that Abraham and Sarah are going through is for them to know God. God is aware when Sarah laughs after he had said that she will have a baby even though Sarah wasn’t there with them. All the circumstances that these two are facing are there to help them know God and trust him. What problems are you facing, what diseases are battling, know that through it all God wants us to know him. So! Will you trust him?