Mulungu amalamulira mbiri ya anthu/God controls human history

Gawani

Luka 2:1-20 tsiku la Christmas ndi tsiku la kubadwa kwa mfumu yodzichepetsa. Ndime yamalembayi ikuonetsa bwino lomwe momwe ulosi wakubadwa kwa mesiya unakwanilitsidwa. Ikutionetsanso kuti obadwayo ndi ochokera ku masiku amake dzana, ndipo ndi mulungu ndithu kubadwira mumbiri ya anthu. Ndime yamalembayi ikuyamba ndi lamulo lochokera kwa Kayisara Augusto. koma ndichifukwa chiyani lamuloli lili lofunika? Tili ndi ulosi kale omwe ukukamba komwe mesiya azabadwire koma n’kuti pa nthawiyi Maria ndi Yosefe akukhala ku Galileya ku Yudeya. Izi zikuonetsa kuti ngati Maria angabereke pa nthawiyi, kuberekako kuchitikira ku Yudeya. Koma mesiya akuyenera kubadwira ku Betelehemu muzinda wa Davide molingana ndi ulosi. Izi ndizofunika kwambiri chifukwa mfumu yodzichepetsayi ikuyenera kuzalowa ufumu wa bambo ake Davide. Kubadwa kudzera mwa Maria ndi Yosefe komanso kubadwira ku Betelehemu zinali zoyenera. Koma kodi zitheka bwanji? Apa ndipamene tingaziwe kuti mulungu mu mphamvu ndi ulamuliro wake amalamulira mbiri ya anthu. Zotsatira zake tikuona Kayesara Augusto akupereka lamulo. Lamulo limeneli lipangisa Yosefe kubwerera kwawo ku Betelehemu pamodzi ndi mkazi wake Maria. Ndipo ali kumeneko ndipamene mesiya akubadwa. Izi zinachitika motere kukwanilitsa malemba ndi ulosi omwe unaneneratu za kubadwa kwa mesiya.   

Luke 2:1-20 the day of Christmas is the day of the birth of a lowly king. This passage paints a clear picture for us as we see a prophecy about the birth of Messiah being fulfilled. It also helps us to understand that the one to be born is from ancient of days. it is God himself being born into human history. Now, the passage begins with a decree made by Caesar Augusto. How is that decree important? We already have a prophecy that tells us exactly where the messiah would be born but at this time we see Mary and Joseph staying in Galilee in Judea. It obviously means that if Mary were to give birth, it would happen in Judea. But the messiah must be born in Bethlehem, the city of David. This is important because the lowly king is to succeed the throne of his father David and his birth through Mary and Joseph and in Bethlehem are just the right circumstances. But how will it happen? This is where we understand that God in his divine providence controls everything. That’s why the decree made by Caesar Augusto is important. This will cause Joseph to go back to his village in Bethlehem obeying the decree. He goes there with his wife and while there it is when Mary gives birth to the lowly king Jesus Christ. This happened to fulfill what was already prophesied about the birth of the messiah.