Mulungu adatumiza mwana wake Yesu amene ali Mulungu ndithu komanso Munthu ndithu.
Yesu sadachimwe ingakhalale tchimo lalingóno.
1 Petro 2:22, “Iye sanachite tchimo kapena kunena bodza.”
Yesu adafela machimo athu.
Aroma 5:8, “Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera.”
Mulungu adaukitsa Yesu kwa akufa.
Aroma 6:9, “Pakuti tikudziwa kuti popeza Khristu anaukitsidwa kwa akufa, Iye sangafenso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye.”