Mwapatulidwa ku Uthenga Wabwino

Gawani

Ndine Paulo, mtumiki wa Khristu Yesu, woyitanidwa ndi Mulungu kukhala mtumwi. Ndinapatulidwa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Mulungu Ndikulembera kwa onse okhala ku Roma amene Mulungu amakukondani nakuyitanani kuti mukhale oyera mtima. Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu. umene analonjeza kale mʼMalemba Oyera kudzera mwa aneneri ake. Uthengawu ndi wonena za Mwana wake amene mwa umunthu wake anali wochokera mwa Davide. Iyeyu ndi amene anatsimikizidwa kukhala Mwana wa Mulungu mwamphamvu za Mzimu Woyera pamene anauka kwa akufa. Kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ife tinalandira chisomo chokhala atumwi oyitana anthu a mitundu yonse kuti amukhulupirire ndi kumumvera mwachikhulupiriro kuti dzina lake lilemekezedwe. Inunso muli mʼgulu la Amitundu oyitanidwawo kukhala ake a Yesu Khristu. Aroma 1:1-7

Mulungu adatipatulidwa ife kuti tikalalikire Uthenga Wabwino ku mitundu yonse kwa ulemerero wa dzina la Mulungu.

You are set apart for the gospel.

Romans 1:1–7. God set us apart to preach the gospel of Jesus Christ to all nations for the glory of God’s name.