1 | Mulungu ndi wabwino

Gawani

Uthenga Wabwino ndi mphamvu za Mulungu zopulumutsa.

Aroma 1:16, “Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino chifukwa ndiwo mphamvu za Mulungu zopulumutsa aliyense amene akhulupirira.”

Nanga Mulungu atati akufunse, “N’chifukwa chiyani ndikuyenera kuti ndikulole kuti ulowe kumwamba?”

Mulungu ndi Mlengi wathu wabwino ndi Mfumu.

Genesis 1:1, “Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”

Mulungu adakulenga iwe kuti ukhale naye komanso ndi kumamukonda iye.

Mateyu 22:37 (Lamulo lalikulu kuponsa onse), “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.”