Mulungu Avumbulutsa Chilungamo ndi Chisomo chake/God reveals his Justice and Grace

Gawani


Genesis 7:1-10, Mmavesi amenewa tikuphunzira za chenjezo lomwe lina pelekedwa munthawi ya Nowa pomwe anthu ankangodya, kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa kufikira Nowa analowa mchombo ndipo chigumula chinabwera. Zomwe ndi chimodzimodzi munthawi yathu lero, pomwe anthu akungodya, kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa. Panthawi yomweyo tikuona za kulungama kwa Nowa komwe kwabwera chifukwa chachikhulupiriro chake pa Mulungu, pomwe anachenjezedwa za chigumula iye anakonza chombo choti apulumutsire banja lake pamodzi naye. Ndipo muzonse Nowa anachita monga momwe Mulungu anamuwuzira.

Genesis 7:1-10, In these verses, we’re learning of the warning given in the days of Noah when the people were only eating, drinking, marrying and being given into marriage, until Noah entered the ark and the door was shut from behind and the flood came. This is the same with our time, people are only eating, drinking, marrying and being given into marriage. At the same time, we’re learning of Noah’s righteousness through faith. when he was given the divine warning, Noah constructed the ark to preserve the lives of his family including his. And in everything Noah did exactly as God commanded him to do.