Mulungu amakwaniritsa malonjezano ake/God fulfils his promises

Gawani

Genesis 10:1-32, mu chaputara chimenechi tikuona ndandanda wa ana a Nowa. Koma nkhani yayikulu yagona pa Semu. Kuchokera kwa Semu kunabadwa mwana yemwe anabereka mwana yemwe anaberekanso mwana yemwe anali tate wa Abrahamu komwe mbewu ya mzimayi ikudzera kufikira pa Yesu Khristu. Mulungu atalonjeza kwa mzimayi uja mumachaputara oyambirira aja za mbewu yomwe izaphwanya mutu wanjoka mubukuli, tikuona kuti akusunga pangano lake pomwe akusunga mbewu imeneyi kudzera mwa Semu. Mulungu amakwaniritsa malonjezano ake.

Genesis 10:1-32, in this chapter we are getting the full detailed genealogy of the sons of Noah and their descendants. But the main story focuses on Shem. It is from Shem where a son was born who gave birth to a son who later on became the father of Abraham through whom the seed of a woman continued until Jesus Christ. After God promised the seed of a woman in the early chapters of this book, God preserves that seed through Shem until Abraham and so on and so forth. God fulfils his promises.