Kupembedza Koona ndi Kuvomereza ndi Mathokozo Chipulumutso cha Mulungu pa anthu ake/A proper worship is a proper response to God’s salvation.

Gawani

Genesis 8:15-22, Nowa akutiwonesera mtima omvera. Nowa anadikira mçhombo ngakhale anali akudziwa kuti madzi adali atawuma ndipo akadatha kutuluka, koma iye anadikira lamuro lochokera kwa Mulungu lomuuza kuti atha kutuluka limodzi ndi ziyama zonse zinali ndi iye mçhombomo. Panthawi yomweyo tikuona kuti chinthu chomwe chikukambidwa mobwereza chokhuza kumvera kwa Nowa ndichakuti iye anachita zonse zomwe mulungu anamulamurira zomwenso ndi chıthünzithunzi cha moyo wa Mesiya. Nowa atatulaka m’çhombo anamanga guwa la nsembe napsereza nsembe ngati njira imodzi yothekozera Mulungu kuti wapulumutsa iye pamodzi ndi banja lake. Mulungu atamva kunukhira kwake kwa nsembeyo anakondwera. Ifenso ngati akhristu tikuyenera kuonetsera mathokozo ndi ulemu kwa Mulungu ngati njira imodzi yopembezera moona, namuthokoza chifukwa cha chipulumutso chomwe tilinacho kudzera mwa Khristu yesu. Nowa anamanga guwa napsereza nsembe pofuna kuthokoza mulungu kamba ka chipulumutso, nafenso anthu tiyeni tipeleke matupi athu ngati nsembe yopsereza kwa Mulungu ngati njira yothokozera mulungu kamba ka chipulumutso ndipo iye azakondwera nafe.

Genesis 8:15-22, Noah shows us a heart of obedience. Noah waited in the ark even though he knew that the water had dried up, he waited for the command from God telling him to get out of the ark along with the animals with him. And as far as the obedience of Noah is concerned, we are told that he did everything that God commanded him to do and he did just so. After he had come out of the ark, he built an altar and offered up a sacrifice to God thanking him for the salvation. When God smelled the aroma of the sacrifice, he was pleased. As true christians we need to show gratefulness and respect to God as way of thanking him for the salvation we have in Christ Jesus. Noah built an altar and offer a sacrifice to God, while as we need to offer our bodies as a living sacrifice and he will be pleased with us.