Moyo wa Chikhulupiriro wa Abrahamu/a life of Faith of Abraham

Gawani

GeneGenesis 22:1-2 ikuyamba ndi yesero. Yesero lomwe ndi lovuta kukwaniritsidwa. Mu vesi yachiwiri ya chaputa chimechi, mulungu akuonetsera momwe kunali kovuta kukwaniritsa yeseroli. Zaka zambiri zadutsa, mulungu wachita zomwe analonjeza kuti achitira Abrahamu. Mulungu wapereka mwana kwa Abrahamu ndi Sara ndipo amutcha Isaki. Mu chaputa 22 cha bukuli tikuona mulungu akumuuza Abrahamu kuti apereke nsembe mwana wake Isaki. Izi zinali zovuta kuchita osati chifukwa Abrahamu anali ndi Isaki yekha (analinso ndi Ishumaeli) koma ndi kudzera mwa Isaki m’mene mulungu adzakwaniritsa ntchito yake ya chipulumutso. Komanso Abrahamu amamukonda Isaki. Abrahamu wavomera kuchita chifuniro cha mulungu. M’malingaliro mwa Abrahamu munali buku la Ahebri lomwe limakamba za chiwukitso. Izi zinapereka mphamvu kwa Abrahamu. Pa ulendo wawo kupita kopereka nsembe Isaki anafunsa bambo ake funso lachodziwadziwa ndipo yankho la funsoli likuonetsera chinthu chofunika chokhuza mulungu. Abrahamu anati “mulungu akapereka.” Pamene Abrahamu amafuna kupha Isaki kuti ampereke nsembe mulungu anamulesa. Ndipo mulungu anapereka mwana wa nkhosa kuti aperekedwe nsembe. Kodi izi zikukamba zotani zokhuza mulungu? Tonse ndi anthu ochimwa amene tikuyenera imfa. Koma mulungu anapereka nsembe osati ya nyama koma ya mwana wake yemwe kuti aphedwe m’malo mwathu. Ngati zotsatira mulungu akupereka chipulumutso kwa anthu ake kudzera mwa mwana wake Yesu Khristu. Kodi inu mukudalira mulungu kapena mumamukaikira? Tiyeni tikhale moyo wa chikhulupiriro momwe anachitira Abrahamu.

Genesis 22:1-2 begins with a test. A test that is too hard to carry out. God in verse two of this chapter makes it clear that all should understand how difficult it is to do what God was asking here. Many years have passed, God has carried out what he had promised. God has given Abraham and Sarah a child and they have named him Isaac. In chapter 22 of this book we see God asking Abraham to do something difficult. He tells him to sacrifice his son Isaac. Now this was difficult for him to do not because Isaac was his only son (he had Ishmael) but was the one through which God would accomplish his plans of salvation. And Abraham loved Isaac very much. Abraham agrees to this and is ready to sacrifice his beloved son. Abraham was strengthened thinking about what is written in the book of Hebrews which says that God has the power to bring someone dead back to life. But something unique happened on his way to sacrifice Isaac. Isaac asks his father an obvious question and the answer to that reveals something important about God. Abraham responds to his son saying “God will provide.” This was not a lie but in fact the truth. When he was about to kill his son Isaac and sacrifice him God stopped him. And he provided a ram for the sacrifice. Abraham had passed the test. What does this say about God? We all are sinners and deserves to die. But God provided a sacrifice of his own son to die in our place and give us his life. As a result, God is giving salvation to his people through Jesus Christ. Do you trust God or are you still doubting him? Let us live a life of faith like Abraham did.