M’busa Watch ndi yemwe anayambitsa Mpingo wa Gospel Life Baptist ndipo amagwira ntchito ndi Euro-Africa Baptist Mission, bungweri liri ku zomba Malawi. Asanayambitse mpingo wa Gospel Life Baptist limodzi ndi Dr. Hutchens, M’busa Watch anali m’busa wa Mpingo wa Baptist ku Phiri la Ntonya kwa dzaka zisanu. Iye ndi mkazi wake Eunice ali ndi ana awiri akazi.

Mbusa Dzimbiri amatsogolera kapembezedwe ku Mpingo wa Gospel Life Baptist komanso amatumikira alimodzi ndi Euro-Africa Baptist Mission yomwe yiri ku Zomba Malawi. M’busa Dzimbiri watumikira mipingo ya ku Malawi komanso ya ku Zambia, ndipo ali ndi M.A. mu maphunziro a zautumiki kuchokera ku Central Africa Baptist University ndi Piedmont International University.

Dr. Hutchens ndi m’busa yemwe anayambitsa Mpingo wa Gospel Life Baptist komanso ndi Mtsogoleri wa Euro-African Baptist Mission, bungweri liri ku zomba Malawi. Dr Hutchens watumikirapo mipingo iwiri mu mzinda wa United States ndipo ali ndi Ph.D. mu maphunziro otchedwa Biblical Theology kuchokera ku The Southern Baptist Theological Seminary. Iye ndi mkazi wake Stacy ali ndi ana asanu.